• Home
    • Advertisement
      Times Courier
  • Daily Times








    • dailytimesAdvertisement
  • Weekend Times
    • Advertisement
      sb
  • Malawi News
    • Advertisement
      qm
  • Sunday Times
    • Advertisement
      steers
  • E-Edition
  • Advertise
  • Contacts

Thu05232013

Last update09:36:16 AM

Back Malawi News Headlines Tikambe

Tikambe

Mwando achotsa chimbenene Perpetual

Italepheleka koyamba nkhonya ya pakati pa Perpetual Mkandawire ndi mnyamata wa ku Zimbabwe Brian Mwando masabata awiri apitawo, Perpetual adakwela pachulu nkunyodola mwa thamo zedi pobwekela kuti Mwando amangonama kuti wadwala litsipa koma chonsecho kuli kuopa zigogodo.

Aphunzitsi ena amalepheretsa dala olumala—Fedoma

Pamela_JumaOphunzira ambiri olumala sukulu za pulayimale m'dziko muno akuti amalephera kusankhilidwa kupita m'sukulu za sekondale zapamwamba chifukwa chakuti aphunzitsi ambiri amanyalanyaza kuwathandiza nthawi imene akulemba mayeso.

Kufa ndi ludzu miyendo ili mmadzi

water-keepNyumba zochuluka zomwe zikupezeka pafupi ndi sukulu ya Kanjedza Primary mumzinda wa Blantyre zimakumana ndi mavuto osowa madzi monganso momwe ziliri mmadera ambiri mumzindamu. Koma izi sizidayenera kukhala choncho mmadera ozungulira sukulu ya Kanjedzayi popeza pafupi pali thanki yaikulu yosungira madzi.

Khonsolo ya Zomba yawonetsa chitsanzo chabwino

M’dziko muno masewero osiyanasiyana akukumana ndi mikwingwirima yosowa thandizo la ndalama kapena zinthu zina zoyendetsera masewerowo. Izi zikuchititsa kuti masewero asamapite m’tsogolo m’dziko muno. Koma nkhani yochititsa chidwi ndi yakuti khonsolo ya Zomba ikuonetsa chidwi chopereka ndalama ku masewero ena monga mpira wa miyendo wa abambo ndi amayi, komanso masewero a hoke.

Kayuni agonja koyamba

Katswiri wa masewero a nkhonya Osgood Kayuni adakumana nazo sabata latha pamene adagonja kwa Wellington Balakasi pamapointi pa nkhonya yomwe idachitika pa Warehouse mu mnzinda wa Blantyre. Kayuni yemwe amadziwika ndikugonjetsa anzake adovomereza za kugonja kwake ndipo wapempha anthu omwe amamukonda kuti asakhumudwe.

Ulendo ulipo mu TNM Super League

Matimu atengetsana chulu chathyula mu mpikisano wa chaka chino wa TNM Super League pomwe timu ya Escom United yomwe ikutsogola ndi mapointi 15 idawona mbwadza mu sabata yachisanu ya mpikisanowu pomwe idabwelera kuchokera ku chigawo cha mpoto chimanjamanja. Escom United yomwe ndi akatswiri omwe akuteteza chikhochi adawona mbwadza pomwe adagonja lamulungu pa bwalo la Mzuzu Stadium ndi timu yatsopano mu mpikisanowu ya Embangweni United pomwe idakhaulitsidwa ndi zigoli ziwiri kwa chimodzi.

Donnas Egg yafika ndime yachiwiri

( ovala zobiliwira) adazisiyaChikho cha mpira wa miyendo wa amayi cha Donnas Egg ku chigawo cha kumwera chafika mundime ya chiwiri pomwe matimu ena azisiya atangonja Sabata latha. Chikhochi chikuseweredwa mudongosolo la kugonja kutuluka (knock out) ndipo matimu monga Topic Super Queens,Young Sisters yaku Balaka, ndi Cobbe Sisters yaku Zomba ndi amene adazisiya. Sabata lino masewerowa ali motere:

Zina ukaona kamba anga mwala

thievesZidali zodabwitsa pa tsiku la 20 Julaye kuona kuti ngakhale amayi adali pakalikiliki wotenga nawo katundu wa sitolo zomwe anthu ena omwe ndi akamatule potengera mwayi pa ziwonetserozo, adayamba kutchola. Zithunzizi zikusonyeza anthu ena mumzinda wa Mzuzu akutenga katundu musitolo ina pa tsikuli.

 

Advertise with us

Advertising that works wonders

Call +2651871181/070/563
or email: advertising@bnltimes.com