Kafukufuku yemwe Tikambe yapanga wasonyeza kuti sikatundu yense yemwe wakwera mtengo kuchokera nthawi imene boma lidalengeza kuti mphamvu ya ndalama ya kwacha yagwa masabata awiri apitawo.
Tikambe idachita kafukufuku m'sitolo zikuluzikulu zogulitsira katunduyo monga za Shoprite, PTC komanso mawokala m'madera a ku mudzi.
Koma bungwe loteteza ufulu wa anthu ogula m'dziko muno la Consumers Association of Malawi (Cama) lati a Malawi asasangalare msanga za nkhaniyi kaamba koti sipatenga nthawi yayitali sitolozo zisadakweze mtengo wakatundu wotsalayu.
Katundu yemwe sadakwelebe mtengo ndi monga buledi, zokumwa zoziziritsa kukhosi, sopo, chimanga ndi mafuta odzola pomwe katundu yemwe wakwera kwambiri mtengo ndi monga shuga, mazira ndi mafuta ophikira.
Mwachitsanzo mafuta ophikira a malita awiri (2litres) adali pa K1,600 koma panopa afika pa K1,900, crate ya mazira yaying'ono idali pa K960 koma panopa yafika pa K1180. Mmadera mwina mtengo wa paketi la Shuga wafika pa K300 kuchokera pa K220 pomwe m'masitolo ena akupanga K250.
Kupatula katunduyo, kafukufukuyo adasonyezanso kuti m'madera ambiri, a eni nyumba akweza kwambiri. Nyumba zina zafika K25,000 kuchokera pa K18,000 pomwe nyumba zina zafika pa K12,000 kuchokera pa K7,500.
Kuthilira ndemanga pa nkhaniyo, a Yohane Bwetule, ochokera m'dera la mfumu yaikulu Chimaliro m'boma la Thyolo adati kukwera mtengo kwa katundu ndi chipsinjo chachikulu chomwe anthu akumidzi sangathe kuchisenza.
"Kudali kofunikira kuti boma lifotokonzere bwino bwino anthu akumudzi za kutsika kwa kwacha komanso kukwera mtengo kwa zinthu m'malo moti tidzingomvera pa wayilesi basi. Mwachisanzo tidali kugona ndi njala katundu asadakwere mtengo, ndiye pano sitikudziwa kuti zitha bwanji," iwo adatero.
A Richard Bandawe, omwe amagwira ntchito pa kampani ina m'boma la Blantyre adati ndizomvetsa chisoni kwambiri kuti katundu wakwera mtengo pamene malipiro ndi omwe aja.
"Chikadakhala chinthu chanzeru kwambiri ngati kukwera mtengo kwa zinthu kukadayendera limodzi ndi kukwera kwa malipiro. Kodi ife tipeza kuti ndalama zogulira zinthu zokwera mtengo pomwe malipiro athu ndi omwe aja," iwo adatero.
Koma a Yusuf Bwanali, a m'boma la Zomba adati Amalawi asade nkhawa kwambiri ndikukwera kwa katundu chifukwa zokoma zili mtsogolo.
"Chofunika pamenepa ndi kungovemereza chifukwa tikapanda kutero ndiye kuti dzikoli tilimva kuwawa. Koma ndili ndi chikhulupiliro kuti posachedwapa zinthu ziyamba kuyenda bwino chifukwa ndamva kuti mabungwe ambiri a kunja ali pikitipikiti kufuna kutithandiza," iwo adatero.
Wamkulu wa bungwe la Cama a John Kapito adati Amalawi asadandaule kwambiri chifukwa pali chikhulupiliro kuti zinthu zidzayamba kusintha komanso kubwelera mu chimake ndalama za kunja zikayamba kubwera m'dziko muno.
"Koma Amalawi ambiri avutika kwambiri ngati ndalama za kunja zichedwa kufika m'dziko muno, choncho tikupempha boma kuti liyesetse kuti ndalama za kunja zabwera msanga m'dziko muno," iwo adatero.
Iwo adati kukwera kwa katundu sichinthu chodabwitsa chifukwa ndi chinthu chimene chimachitika dziko lirilonse ndalama ikatsika mphamvu.
"Katundu yemwe sadakwere mtengoyo akwera pasachedwa, mwina makampaniwo akungodikira kuti achite ndondomeko yoyenera," iwo adatero.
Kupatula katundu ndi nyumba, mitengo ya magetsi ndi mafuta yakwelanso mtengo, zomwe zapangitsa kuti mitengo ya minibasi ikwelenso.

Advertisement







