• Home
    • Advertisement
      Times Courier
  • Daily Times








    • dailytimesAdvertisement
  • Weekend Times
    • Advertisement
      sb
  • Malawi News
    • Advertisement
      qm
  • Sunday Times
    • Advertisement
      steers
  • E-Edition
  • Advertise
  • Contacts

Tue05212013

Last update05:07:43 PM

Back Malawi News Headlines Tikambe Sindisunga mangawa—Pulezidenti Banda

Sindisunga mangawa—Pulezidenti Banda

President_Joyce_Banda_signing

Pulezidenti Joyce Banda wati sasunga mangawa aliwonse kuchokera kwa munthu wina aliyense zomwe akhala akumunena, koma maso akhale kutsogolo kukonza dziko lino. Iye adalankhula izi Loweruka lapitali pomwe amamulumbiritsa ku Nyumba ya Malamulo ku Lilongwe.

"Ndilibe mangawa ndi munthu aliyense. Tiyeni tigwire ntchito yotukula dziko lino," adatero Pulezidenti Banda.

Mtsogoleri wa Malawi Congress Party (MCP) John Tembo wapempha a Banda kuti choyamba ayenera kuchotsa mabilo osafunikira kwambiri kwa Amalawi omwe aphungu aku Nyumba ya Malamulo adavomereza masiku apitawa.

Iye adati pali mabilo amene aphungu adavomereza opanda kufunsa anthu awo zomwe adati nzosathandiza konse.

"Mwachitsanzo; pali bilo yopatsa nduna mphamvu kutseka nyumba yolemba nkhani (Section 46), komanso bilo yoletsa ziletso (Injunction Bill). Aphungu otsutsa boma tidzathandiza kupereka mfundo zothandiza boma. Pulezidenti Banda asade nkhawa tigwira naye ntchito limodzi," adatero Tembo, yemwe ndi mtsogoleri wa aphungu otsutsa boma m'Nyumba ya Malamulo.

Mtsogoleri wa Nyumba ya Malamulo, George Chaponda wati kusankhidwa kwa Banda kwatsimikizira kuti anthu m'dziko muno akutsata konstitushoni ya dziko lino.

"Ife monga a DPP takonzeka kugwira ntchito limodzi ndi boma palibe chovuta, chifukwa tonse tikufuna kutukula dziko lino," adatero Chaponda.

Koma mtsogoleri wa aphungu a UDF m'Nyumbamo, Ibrahim Matola adati palibe chovuta, koma sadakumane kuti azidzagwira bwanji ntchito.

"Padakali pano sitidakumane, koma ndikuyankhani tikakumana," adatero Matola Lolemba.

Kachenjede pa za malamulo ku Chancellor College, Edge Kanyongolo wati, chinthu choyambirira chimene Pulezidenti Banda achite nkukonza ubale wa mayiko amene amathandiza dziko lino pa chuma, komanso pa chitukuko, kuyanjanitsa ubale wa mayiko oyandikana nawo, kenako akonze za mavuto a kusowa kwa ndalama za kunja ndi kusowa kwa mafuta kumene kwagwededza dziko lino.

"Pali mayiko amene akhala akutithandiza kwa zaka zambiri, koma adasiya malinga ndi zifukwa zina, choncho ndi udindo wa Pulezidenti kukonza zimenezo," Kanyongolo adatero.

Padakali pano akuluakulu a bungwe la Malawi Confederation of Chambers of Commerce and Industry (MCCCI) ndi Press Corporation Limited (PCL) ati ali ndi chiyembekezo kuti ubale umene udalipo ndi mayiko amene amathandiza dziko lino uyambiranso.

Mkulu wa bungwe la zamalonda la MCCCI Mathews Chikankheni wati mavuto m'dziko muno ndi ambiri, komabe anthu ali ndi chiyembekezo kuti mavuto omwe dziko lino akukumana nawo achepa.

"Aliyense akudziwa mmene zinthu ziliri m'dziko muno, koma zongofuna kuziwunika bwino," Chikankheni watero.

Naye mkulu wa kampani ya Press, a Mathews Chikaonda wati pamene Pulezidenti Banda azisankha nduna za boma awonetsetse kuti asankhe anthu okhawo amene angathe kumuthandiza kuyendetsa boma.

 

Advertise with us

Advertising that works wonders

Call +2651871181/070/563
or email: advertising@bnltimes.com