• Home
    • Advertisement
      Times Courier
  • Daily Times








    • dailytimesAdvertisement
  • Weekend Times
    • Advertisement
      sb
  • Malawi News
    • Advertisement
      qm
  • Sunday Times
    • Advertisement
      steers
  • E-Edition
  • Advertise
  • Contacts

Thu05232013

Last update04:07:55 PM

Back Malawi News Headlines Tikambe Mabungwe, matimu amasewero alira Bingu

Mabungwe, matimu amasewero alira Bingu

Hellen_Mpinganjira

Mabungwe kuphatikizapo matimu amasewero osiyana siyana m'dziko muno ati ndi okhudzidwa kwambiri ndi imfa ya mtsogoleli wakale wa dziko lino a Bingu Wa Mutharika omwe adamwalira mwadzidzi sabata latha.

Polankhula ndi Tikambe mwapadera padera sabata ino, atsogoleli a mabungwe komaso matimu a masewero osiyana siyana adati dziko la Malawi lataya munthu ofunikira kwambiri yemwe adali ndi chidwi chothandiza kutukula masewero m'dziko muno kudzera mu ndondomeko yomwe pachingerezi imadziwika kuti Presidential Initiative on Sports. Koma atsogoleliwo adafotokoza kuti ndichikhulupiliro chawo kuti mtsogoleli watsopano wa dziko lino a mayi Joyce Banda apitiliza kutukula masewero m'dziko muno.

"Imfa ya mtsogoleli wakale wa dziko lino a Bingu Wa Mutharika ndi chiphinjo chachikulu kuchitukuko cha masewero a mpira wa miyendo m'dziko muno popeza ndondomeko yake ya Presidential Initiative on Sports imathandiza kutukula luso lachinyamata m'dziko muno. Koma popeza ndondomekoyi idakhazikitsidwa mu ofesi ya president, tili ndichikhulupiliro chonse kuti zinthu zipirilira kuyenda bwino," adatero a Suzgo Nyirenda, yemwe ndi mkulu wa bungwe la FAM.

Pofuna kupeleka ulemu kwa mtsogleli wa kale wa dziko linoyu, mipikisano ya masewero osiyana siyana m'dziko muno idayimitsidwa kaye ndi akulu akulu kuchokera sabata latha. Ndipo masiku omwe masewerowo adzayambike awalengeza pasachedwapa, kweni kweni thupi la mtogoleli wakale wa dziko lino likayikidwa m'manda.

Malingani ndi wapampanda wa gulu lomwe likuyendetsa za mwambo onse wa maliro wa mtsogoleli wakale wa dziko lino a Henry Mussa, mtsogoleli Bingu Wa Mutharika adzalowa m'manda pa 23 mwezi omwe uno ku munda wake wa Ndata m'boma la Thyolo.

M'mawu ake, mlembi wamkulu wa bungu la Boxing Association of Malawi a Arthur Nanthuru adati imfa ndi chinthu chowawa kwa munthu komaso mtundu uliwonse.

"Imfa ndichinthu chomwe munthu aliyense sayembekezera pakati pathu. Kotero kuti kutaya kholo ngati mtsogoleli wakale wa dziko lino ndikowawa kwambiri kaamba koti adali ndi ntchito yotamandika yo tukulu masewero osiyana siyana m'dziko muno," adatero a Nanthuru.

Mlembi wamkulu wa Netball Association of Malawi (NAM) a Hellen Mpinganjira adati kupatula kuchitukuko cha masewero osiyana siyana m'dziko muno, imfa ya mtsogoleli wa kale wa dziko lino ndi nkhani yomvetsa chisoni kwambiri kwa zika iliyonse ya Malawi.

"Pa umunthu, imfa ya mtsogoleli wakale wa dziko lino ndi nkhani yodzidzutsa komaso yomvetsa chisoni kwambiri chifukwa choti sitimayembekezera kuti tingataye kholo lathuli. Koma poti ndichikonzero cha Mulungu, tingoti Namalenga odziwa kuonthoza afungatire banja lake komaso mtundu wa a Malawi," adatero a Mpinganjira.

A Mpinganjira adati ali ndichikhulupiliro chonse kuti mtsogoleli wa tsopano wa dziko lino mayi Joyce Banda apitiliza ntchito yotukula masewero osiyana siyana m'dziko muno, pofotokoza kuti banja lawo lili ndi chidwi cha masewero.

"Mtsogoleli wa dziko lino wakhala akuonetsa chidwi chotukula lusa la masewero la achinyamata popeleka mwayi wa maphunziro kwa anyamata komaso atsikana pa sukulu yake ya Joyce Banda Foundation mumzinda wa Blantyre. Kotero ndizosakaikitsa kuti mayi athuwa apitiliza kutukula masewero m'dziko muno kaamba ka chidwi chawo," adatero a Mpinganjira.

Koma a Mpinganjira adati tsogolo la timu yake ya Bingu Tigresses ndilomwe silikudziwika bwino kaamba ka imfa ya Bingu Wa Mutharika yemwe ankayithandiza.

Pamene mphunzitsi wa timu ya Red Lions a Collins Nkuna adafotokoza kuti Mtsogoleli wa kale wa dziko lino adzakhala akukumbikilidwa kaamba ka zipatsa zabwino za ndondomeko ya Presidential Initiative on Sports yomwe yathandiza matimu ambiri kupindula munjira zosiyana siyana.

 

Advertise with us

Advertising that works wonders

Call +2651871181/070/563
or email: advertising@bnltimes.com