• Home
    • Advertisement
      Times Courier
  • Daily Times








    • dailytimesAdvertisement
  • Weekend Times
    • Advertisement
      sb
  • Malawi News
    • Advertisement
      qm
  • Sunday Times
    • Advertisement
      steers
  • E-Edition
  • Advertise
  • Contacts

Sat05252013

Last update04:07:55 PM

Back Malawi News Headlines Tikambe Nanazi zikusintha miyoyo ku Mulanje

Nanazi zikusintha miyoyo ku Mulanje

M'phephete mwa phiri la Mulanje kungoyenda pang'ono kuchokera mu nkhalango ya tiyi ya Minimini kuli mudzi waukulu wa Nande. Mudziwu, womwe wapangidwa ndi midzi ina yaing'onoing'ono monga Kholowa, Munyaka, Gawanya ndi ina, umabiriwira nthawi zonse ndi mbewu zosiyanasiyana zomwe anthu a mderali amalima.

Zina mwa mbewuzi ndi tomato, nthochi ndi nanazi. Nanazi ndi zimene zimalimidwa kwambiri moti midzi ya Nande ndi Nessa imadziwikanso ndi maina oti ''Midzi ya Vinanazi''. ''Vinanazi'' ndi mau ochokera ku nanazi mu chiyankhulo cha chi Mang'anja. Anthu ambiri a m'midzi iwiriyi-Midzi ya Vinanazi-ndi a mtundu wa chi Mang'anja.

Ulimiwu umagwirizana ndi nyengo ndi nthaka ya mderali. A Aubrey Pensulo, mlimi wa nanazi ochokera kwa Kholowa, adati nanazi ndi golide kwa alimi a Nande ndi Nessa.

Mau a Pensulo amalasa mtima munthu ukangoyang'ana kwambiri pa zaumoyo wa anthu a ''M'midzi ya Vinanazi''. Nyumba zomangidwa mwa makono zazungulira m'midziyi ndipo makomo ambiri ndi a mwanaalirenji.

Zonsezitu zikuchokera mu ulimi wa nanazi.

A Pensulo, omwe akhala pa ulimi wa nanazi kwa zaka khumi, amapeza ndalama zosachepera K50,000 pa chaka."M'mbuyomu ndimakonda kumaunyoza ulimi ndikumataya nthawi yanga ku ma esiteti a tiyi. Pano moyo wanga wonse uli mu nanazi,"akutero a Pensulo.

Nawonso a Donnex Yaiwa am'mudzi wa Nessa ali odzala ndi chimwemwe chifukwa cha ''golide''wobisikayu. "Nanazi zimandipindulira kwambiri kusiyana ndi tiyi. Moti pali ganizo loti ndizazule mbewu ya tiyi ndi kubzala nanazi,"akutero a Yaiwa a zaka 52. Kupatula nyumba yopatsa kaso iwowa alinso ndi zifuyo zambiri. Koma ganizo lozula tiyi n'kubzala nanazi ndi lanzeru?

A Estere Kadam'manja a m'mudzi woyandikana ndi wa Michenga kwa T/A Mabuka komweko akutsutsa. "Nanazi zikutukula miyoyo ya anthu kuno;tiyi akutukulanso miyoyo ya alimi ang'onoang'ono choncho ndibwino kumalima zonse,"mayi Kadam'manja,omwe amuna awo adamwalira kalekale, adauza Tikambe.

Mayiwa akuvomera kuti nanazi ndi zimene zasintha moyo wawo.

Kupatula kugulitsa nanazi alimi akugulitsanso mbewu ya nanaziyi yomwe ena amaitcha kuti nsakazi. Nsakazi zimagulitsidwa pa mtengo wa K30 pa nsakazi ina iliyonse. Ogula amachoka ku unduna wa za ulimi ku Thyolo ndipo ena amachokera ku Mzuzu chigawo chakumpoto.

Mlangizi wa boma pa nkhani za ulimi mderali a Martin Kaponda akuvomereza kuti alimi a nanazi akupinduliradi pa zaulimi wawo. Koma iwo adalangiza alimiwa kuti apeze msika wabwino ndi wokhazikika kuti azipindula kwambiri.

M'zaka zapitazo alimi ena amadalira msika wa Mulanje Peak Foods yomwe idali nthambi ya kampani ya Dairibord Malawi Limited. Msikawu udatsekedwa miyezi yapitayo malingana ndi kulongosola kwa akuluakulu a kampaniyi mu nyuzipepala ya Daily Times.

Komabe alimi monga a Pensulo akuti sakukhumudwa kwenikweni ndi nkhaniyi.

"Tipitilizabe kugulitsa nanazi zathu kumitsika monga Mini-mini, Mulanje Bus Depot, Chitakale ndi ina yotero,"akutero a Pesulo a zaka 33.

Boma la Malawi lilipakalikiliki wofufuza mbewu zodalirika zomwe zingalowe m'malo mwa fodya yemwe tsogolo lake lili mumdima. Akatswiri a zachuma akhala akunena kuti fodya sangasinthidwe ndi mbewu imodzi yokha koma mbewu zambiri monga tiyi, thonje, nandolo ndi zina.

 

Advertise with us

Advertising that works wonders

Call +2651871181/070/563
or email: advertising@bnltimes.com