• Home
    • Advertisement
      Times Courier
  • Daily Times








    • dailytimesAdvertisement
  • Weekend Times
    • Advertisement
      sb
  • Malawi News
    • Advertisement
      qm
  • Sunday Times
    • Advertisement
      steers
  • E-Edition
  • Advertise
  • Contacts

Fri05242013

Last update04:07:55 PM

Back Malawi News Headlines Tikambe Mawira: Dziwe la madzi otentha

Mawira: Dziwe la madzi otentha

Mawira_Hot_Water_Springs

M'boma la Nkhotakota m'mudzi mwa Tambala m'dera la Mfumu Malengachanzi muli malo ena amene amatulutsa madzi otentha ndipo anthu adawatcha malowa kuti Mawira (kutanthawuza madzi otentha). Anthu ena makamaka amayi mmalo mophitsa madzi oti amuna awo asambe amangopita kukatunga nkuyika ku bafa, kodi nanga chiyambi chake nchotani. Mfumu Malengachanzi ikufotokoza za chiyambi cha mawira motere:

Kodi Mawira adayamba bwanji?

Tsikulo kutacha anthu adangowona chiphalaphala (vokano) cha madzi chikututumira, kenako adayitanizana kuti adzawone chimene chikuchitika. Ndipo anthu aja adayesera kuti adziwe kuzama kwa dzenjelo pozika msungwi zazitali koma osapeza kuzama kwake kenako adangosiya, koma patatha masiku angapo chiphalaphala chija chidasanduka madzi, koma otentha.

Kwenikweni chidachitika nchiyani kuti mpaka chiphalaphala chisandukenso madzi?

Bambo, zolengedwa ndi Mulungu ndi zovutirapo kuzimvetsa, ndipo palibe angazimvetse. Amfumu, mpaka kuzikhumatitsa kuti 'akuti' popeza ntchito yanu ndiyodziwitsa anthu zachikhalidwe ngati zimenezi. Eee! Palibe kanthu mwina pali anthu ena adamvera mwina koma zimene ndakambazi ndi mmene makolowo adandiwuzira, chifukwatu munthu ukalowa ufumu umayenera kudziwa mbiri ya chinthu chirichonse m'deralo kapena m'bomalo, koma muyenera kumvetsa, kuti ndidachita kuwuzidwa ndi makolo anga. Ndinganene kuti limenelo ndi kale kwambiri dziko lino liri mphonje, chifukwa zidachitika atsamunda asanalowe m'dziko muno, ndiye mungathe kudziwa nokha kuti ndi zamizimu. Mwachidule; ndidakati 'mawira' ndi madzi ochokera ku mizimu.

Tsono adamanga mpanda uja ndani?

Nthawi! Zikumveka kuti atsamunda atatulukira malowa adayamba kumakachezapo kenako adaganiza zowateteza kwa ana kapena anthu oledzera kuti mwina angagweremo, ndiye adamanga mpanda wa njerwa kuzunguliza dzenjelo, kenako atawona kuti anthu ena makamaka abambo ankasambira pa mtetete, adamanganso mabafa kuti anthu azisambiramo. Zangokhala zovuta kuti anthu ena adaphwasula mabafawo monga mwawonera, koma amathandiza kwambiri.

Tsono munthu akafuna kusamba amatani?

Apo ndiye ndiyankha bwino kaamba koti zikuchitikabe ndipo ndimapeza anthu akutunga kapena kusamba madzi, makamaka ndikadzera njira zodutsa kuyendera mudzi wanga. Zikukhala ngati mwadzera njira yomweyo pobwera kuno. Munthu akafuna kusamba amatunga madziwo, kaamba kakuti pali mpope wotulukira ndiye amangotchezekera basi kutenga kukasamba, ngati amutenthera kwambiri malinga ndi mmene akufunira amasakaniza ndi ozizira, chifukwa mpope womwewo kunsi kwake kumakhala madzi ozizira—zodabwitsa bambo. Koma chokhumudwitsa nchoti boma likukhala ngati silikulabadira kukonza malowa, chifukwa munthu kubwera kuno ku Nkhotakota osafika pa mawira ndiye kuti wasemphana ndi zinthu zachilengedwe. Ngakhale adamanga mpanda, koma adabowola malo ena oti anthu azitchezekerapo zidebe zawo mmalo moti azitunga polowetsa zidebe padzenjepo kuwopa kugweramo.

Popeza kuti palibe denga, bwanji mvula ikamagwa madziwo samazizira?

Ayi, mudakafikapo mvula ikugwa mudakapezabe nthuzi iri tukutuku, palibe kuti mvula ikugwa madzi azizira ayi, sawona kuti kuli mvula kapena dzuwa kutentha kwake nchimodzimodzi nthawi zonse. Ndatitu zopangidwa ndi Mulungu palibe angazimvetse—ndi za mizimu, kudakakhala kotheka ndidakati; m'boma lino tadala, kaamba koti m'mudzi mwa Kafozera pali malo otchedwa Kasitu, Mwalamtondo-m'mudzi mwa Mchemera komanso kwa Mfumu Mphonde kuli malo ena amawatcha Chombo, koma malo otchuka kwambiri ndi mawira. Mawira ali pamtunda wa pafupifupi makilomita awiri kuchokera pa mseu watala wochoka ku Salima, musanafike pa boma chakumanzere.

 

Advertise with us

Advertising that works wonders

Call +2651871181/070/563
or email: advertising@bnltimes.com