Warning: fopen(/home/starc2/public_html/t3-assets/6d68a86da7c6e4b7c4983f5c91334477txt) [function.fopen]: failed to open stream: No space left on device in /home/starc2/public_html/plugins/system/jat3/core/head.php on line 427
Batile lisowa pa siteji ya Kawale
  • Home
    • Advertisement
      Times Courier
  • Daily Times








    • dailytimesAdvertisement
  • Weekend Times
    • Advertisement
      sb
  • Malawi News
    • Advertisement
      qm
  • Sunday Times
    • Advertisement
      steers
  • E-Edition
  • Advertise
  • Contacts

Thu05232013

Last update04:32:58 PM

Back Malawi News Headlines Tikambe Batile lisowa pa siteji ya Kawale

Batile lisowa pa siteji ya Kawale

Zinthu zina zikamachitika zimangokhala ngati nkhamba kamwa chabe. Pajatu sabata latha mkuluyu adakumana ndi mbwadza pomwe atsinzinantole ena adamubera chigubu cha mafuta pa siteji ya pa Mchesi pa ulendo wa usiku olowera ku Area 23. Itanyamuka pa Mchesi, minibasiyo idaimanso pa siteji ya pa Kawale 1. Shasha ndi dalaivala wakeyo adali kulirabe chifukwa chobetsa mafuta.

Dalaivalayo adapitilira kudzudzula kondakitala wake chifukwa chogona pa ntchito.

"Iwe amakubera bwanji chigubu cha mafuta utakhala pompa?" Iye adakalipa. Shasha adafuna kuyankhapo: "komatu pamene ine ndimati..." Mauwa sadawamalize popeza dalaivalayo adamudula pakamwa: "Usandikweze BP wamva! Khala chete! Udzachangamuka liti?" Adatero dalaivalayo akutsika minibasiyo ndipo kenaka adazungulira kuchitseko mbali yomwe Shasha adakhala.

"Iwetu undiphulitsa ngozi!" Adanenetsa dalaivalayo akupinda malaya. Mmene amati ayambe zigogodo mapasenjala ena adaleletsa ndipo adamugwira dalaivalayo kwinaku nayenso Shasha akunjanjanjanja: "Inetu ndikhonza kukusiyira minibasiyi nkutenga ndalama zonse zomwe tapanga lero!" Shasha adatero diso liri pamtunda.

Mapasenjala omwe adatsika pa malowa adali atabalalika ndipo padatsala okhawo omwe amapitilira ndi ulendowu. Kenaka dalaivala uja adabwelera ku malo kwake koma mmene amati alize minibasiyo idakana kulira. "Tagunditsa mateminolowo!" Iye adalamula. Chomwe amatanthauza pamenepa chidali choti Shasha agwiregwire malo omwe mawaya ena awiri opereka mphamvu zolizira galimotolo amalumikizana ndi batile la minibasiyo.

Shasha adavundukula lata pomwe pamakhala batile. "Aaa!!" Iye adakuwa ngati walumidwa ndi nankalizi ndipo adaonjeza, "palibetu batile apa!" Thupi la dalaivala uja lidauma. Sadakhulupilire mpang'ono pomwe. Poti mminibasiyi mudali mdima kaamba kopanda magetsi, dalaivalayu adadumpha pa mpando wake nkuyamba kupapasa pomwe pamakhala batilepo.

Mawu adakanika kuturuka ngakhale adatsekula pakamwa. "Mwabetsanso batile! Inu nde kaya ndithu! Sindidaone shoveli ndi accountant wake ombwambwana ngati inu!" Pasenjala wina adakuwa. Nthawiyi nkuti mapasenjala ambiri adali atabanika nkuseka. "Kodi awirinu...tauniyi mwaiyamba pompano eti? Tibwenzereni ndalama zathu... muzipanga za batile zanuzo!" Pasenjala wina adalamula ndipo mosakhalitsa padabuka kusamvana Shasha atakana kubwenza ndalamazo makamaka kwa mapasenjala otsikira siteji ya pafupi ya Kawale 2.

"Ukalimbikira zoti subwenza za otsikira pa Kawale 2 ife ndiye ulanditsa injini!" Wina adaopseza.

 

Advertise with us

Advertising that works wonders

Call +2651871181/070/563
or email: advertising@bnltimes.com