• Home
    • Advertisement
      Times Courier
  • Daily Times








    • dailytimesAdvertisement
  • Weekend Times
    • Advertisement
      sb
  • Malawi News
    • Advertisement
      qm
  • Sunday Times
    • Advertisement
      steers
  • E-Edition
  • Advertise
  • Contacts

Sun05192013

Last update04:23:09 PM

Back Malawi News Headlines Tikambe ‘Alimbikitsa ulimi wa nthilira’

‘Alimbikitsa ulimi wa nthilira’

Mlimi_wa_chimanga

Alimi a m'boma la Rumphi awalimbikitsa kuti ayambe ulimi wothilira pamalo amene akhoza kuchita ulimiwu.

Mkulu wa za ma pulani ndi chitukuko m'boma la Rumphi a Frank Mkandawire ndi amene analimbikitsa alimiwa Lachisanu lapitali pamene akuluakulu a unduna wa za malimidwe, ulimi wothirira ndi chitukuko cha madzi amapereka ma sikimu awiri kwa anthu a m'bomali.

A Mkandawire anati m'boma la Rumphi muli malo opitilira 220,000 hekitazi oti akhoza kugwiritsidwa ntchito pa ulimi wothirira, koma ndi malo 6,000 hekitazi okha amene akugwiritsidwa ntchito pa ulimiwu.

"Ndi za chisoni kuti ndi malo ochepa okhawa amene akugwiritsidwa ntchito pa ulimiwu," anatero a Mkandawire omwe anaimira Bwana mkubwa wa boma la Rumphi pa mwambowu.

"Mukhoza kugwiritsa ntchito malo ochuluka pa ulimi wothirira ndi kupeza ndalama za nkhani nkhani zomwe zikhoza kusintha moyo wanu wa tsiku ndi tsiku."

A Mkandawire anati mwachitsanzo alimi akhoza kulima tomato ndi mbeu zina zimene akhoza kugulitsa ndi kudya nasintha miyoyo yawo.

Masikimu amene amaperekedwa pa tsikulo ndi a Tiyese ndi Tapukwa komwe alimi akulima, mwa zina, chimanga, matimati, mbatata ya kachewere, nyemba ndi soya.

 

Advertise with us

Advertising that works wonders

Call +2651871181/070/563
or email: advertising@bnltimes.com