Omwe akupereka ndalama yoyendetsera chikho cha Matindi Academy alonjeza kuti chaka chino chikhocho ndalama yake ikwera kuchoka pa K1.5 miliyoni kufika pa K3 miliyoni.
Izi zidalankhulidwa Sabata latha la Mulungu pa bwalo la masewero la Chiwembe ndi a Madalitso Mpaso omwe adaimira eni ake a Matindi Academy pamene timu ya Matindi Academy imalandila chikho itangonjetsa Poly Ladies ndi zigoli zitatu kwa du.
"Ife a Matindi timakhulupilira kuti sukulu sinkalasi mokha komanso zochita zosiyanasiyana monga masewero, ndiye chifukwa chake tadaganiza zoyambitsa chikhochi.
"Chikhochi chipitilira kuseweredwa mwakuti ndalama yake taikweza kuchoka pa K1.5 miliyoni kufika pa K3 miliyoni," a Mpaso adatero.
Ndipo pulezidenti wa mpira wa miyendo wa amayi m'dziko muno a Suzgo Ngwira adathokoza a Matindi potenga mbali yothandiza mpira wa miyendo wa amayi m'dziko muno.
"Ndikufuna kuthokoza sukulu ya Matindi Academy pokhala ndi chidwi ndi masewero a mpira wa miyendo wa amayi.
"Pambali poyambitsa chikhochi sukulu ya Matindi ikulipirira atsikana ena msukulu zawo zomwe ndizonyaditsa komanso zalimbikitsa maphunziro a atsikanawo omwe ena mwa iwo adasiya sukulu,"a Ngwira adatero.
Timu ya Matindi Academy idalandira ndalama zokwana K200,000 pokhala akatsiwiri pamene Poly Ladies idalandira K100,000, Namalimwe yomwe idakhala yachitatu idapukuta misozi ndi K75,000, ndipo Saint Louis idachoka ndi K50,000.

Advertisement







