Achinyamata amatengedwa kuti ndi atsogoleli amawa, koma kaamba kazovuta zomwe amakuna nazo pa moyo wawo watsiku ndi tsiku iwo amalephera kukwaniritsa masomphenya awo m'moyo. Mwachitsanzo, malingaliro awo odzakhala nzika zodalilika za dziko lino mtsogolo muno monga anamwino, atolankhani, asungi chuma komaso oweluza nkhani kumabwalo a milandu amamathera m'mlengalenga kaamba kazovuta zomwe amakumana nazo.
Malinga ndi kafukufuku, kutenga pakati posayembekezera, mulili wa HIV ndi EDZI, umphawi komaso makhalidwe oipa ndi zina mwa zoletsa zambiri zomwe zimasokoneza chitukuko cha achinyamata m'dziko muno.
Koma ngati njira imodzi yofuna kuonetsetsa kuti ufulu wa atsikana ukulemekezedwa m'dziko muno, Bungwe lotchedwa Girls Empowerment Network layamba kulimbikitsa ntchito yotukula miyoyo ya atsikana m'jira zosiya siyana ngati kumva madandaulo amavuto akulu akulu omwe atsikana amakumana nawo m'madera awo m'dziko muno.
Ndipo ntchitoyi yayambika m'maboma a Blantyre ndi Chiradzulu masabata awiri apitawo. Malingana ndi mkulu ofalitsa nkhani za bungwe la Girls Empowerment Network a Memory Banda, ntchito yolimbikitsa ufulu wa atsikanayo ikuchitika m'magawo awiri: kuthetsa mchitidwe okwatitsa ana ang'ono komaso kulimbikitsa atsikana kuti akhale odzidalira paokha.
"Ndondomeko yothetsa mchitidwe okakamiza ana ang'ono kukwatiwa tayikhazikitsa m'boma la Chiradzulu komwe mchitidwe okwatitsa ana wakakata kwambiri kaamba ka chikhalidwe komanso zikhulupiliro zamakolo zoipa. Pamene gawo lolimbikitsa atsikana kuti akhale odzidalira paokha likuchitika ponseponse. Koma pakali panopa ntchitoyi yakakati m'boma la Blantyre," adafokoza chomwechi a Banda.
Malingana ndi a Banda, atsikana ambiri m'dziko muno ali pachiopsezo chokumana ndi mavuto owopsa m'moyo mwawo ngati kutenga kachilombo koyambitsa mulili wa Edzi ngati sakusamalira mayendedwe awo.
"Sizochita kubisa masiku ano kuti chomwe chikuononga tsogolo la a tsikana ambiri ndi mimba zosayembekezera komanso mulili wa Edzi. Kotero atsikanawa akapanda kudziwa ubwino wopewera zinthu ziwirizi pa moyo wawo ndiye kuti chitukuko cha moyo wawo sichingayende. Pa chifukwa ichi, tidachiona chinthu cha mzeru kuti tiyambe misonkhano ya zokambirana mavuto omwe atsikanawa amakumana nawo m'dziko muno," adatero a Banda.
Mwazina, misonkhano ya atsikanayo imapeza zovuta zomwe atsikana ambiri akukumana nawo m'dziko muno ndinso kukambirana njira zomwe angawathetsere. Chiyambileni ndondomekoyi, misonkhano ya atsikanawo yakhala ikuchitika m'madela ngati sukulu ya sekondale ya Zingwangwa komanso Soche Tourist Lodge mumzinda wa Blantyre masabata atatu apitawo ndipo adasonkhanitsa achinyamata oposa 700 komaso atsikana okwana 150.
Chulungamo ndi chakuti mabungwe ambiri m'dziko muno amadziwika bwino ndi ntchito zomenyera ufulu wa anthu ovutika. Koma funso nkumati: kodi Girls Empowerment Network ikakonza misonkhano yolimbikitsa atsikanawo zimathero pomwepo basi ngati momwe mabungwe ambiri amachitira?
"Sichoncho iyayi, cholinga chathu ndikufufuza zovuta zomwe atsikana anthu amakumana nawo komanso kupeza njira zochepetsera mavutowo. Mwachitsanzo, atsikana ena timawathandiza ndi ndalama zoti ayambire bizinesi zing'ono zing'ono," adatero a Banda.
Malingana ndi a Banda, chida chodalilika pa khalidwe la atsikana ndi kukhala odziletsa ku makhalidwe omwe angawabweretsere mavuto ngati kutenga pathupi.
"Zimakhala zomvetsa chisoni kwambiri kuona atsikana ena akukhala nawo m'misonkhano yathu koma kumbali ndikumakapitiliza kuchita makhalidwe oipa. Koma kudziretsa komanso kukhala ndi cholinga cheni cheni chofuna kudzachikwanilitsa m'moyo ndi njira imodzi yomwe ingateteza atsikana kumavuto osiyana siyani chifukwa chisankho chawo ndiye chida chodalirika," adatero a Banda.
Pa zazikhulupiliro komanso zikhalidwe zomwe zimalimbikitsa ma ukwati ana m'dziko muno, a Banda adati mafumu ali ndi udindo ochitapo kanthu kuti izi zitheleretu m'dziko muno.
"Mafumu amadziwa kuti miyambo ina yosakhala bwino imachitika m'madera awo koma safuna kuchitapo kanthu. Koma adziwe kuti izi zimabwezera m'buyo chitukuko cha dziko chifukwa ana omwe amakwatiwa asanapange maphunziro amakhala alibe chinthu chomwe amachita kuti atukule miyoyo yawo. Kotero ndi umphawi wadzaoneni omwe umatsatira nthawi zonse," adater a Banda.

Advertisement







