• Home
    • Advertisement
      Times Courier
  • Daily Times








    • dailytimesAdvertisement
  • Weekend Times
    • Advertisement
      sb
  • Malawi News
    • Advertisement
      qm
  • Sunday Times
    • Advertisement
      steers
  • E-Edition
  • Advertise
  • Contacts

Sun05192013

Last update04:23:09 PM

Back Malawi News Headlines Tikambe Kondaine: Mankhwala odyetsa amuna

Kondaine: Mankhwala odyetsa amuna

Kukambilana_za_Edzi

Masiku apitawa ndidakhala nawo pa zokambirana zokhudza matenda a Edzi m'boma la Neno, padali magulu angapo kotero kuti gulu lirilonse linkakambirana zokhudzana ndi kufala kwa Edzi, ena adati Edzi ikufala kaamba koti amuna kapena akazi ena amasiya maanja awo nkumachita zachisembwere. Pamene gulu lina lidati pali akazi ena amakonda kudyetsa amuna a eni kondaine. Choncho ndidafunsa Gogo Elina Kankhuni omwe adali m'gulu lokambirana za kondaine. Iwowa amachokera a m'mudzi mwa Donda II m'dera la Mfumu Chekucheku.

Nkhani yakula apa ndi ya kondaine, kodi ndi kanyama kanji?

Achimwene, kondaine ndi mankhwala owopsa kwambiri, akazi ena amakonda kudyetsa amuna awo kuti aziwakonda. Nthawi zina mkazi akachita chibwenzi ndi mwamuna woti ali kale pa banja, ndipo akufuna kulanda amafuna kondaine kapena khudzumule nkumudyetsa, ndipo amazunguliradi mutu. Nthawi zina amachita izi kuti mkaziyo azikhala ngati mkulu m'banjamo, oti kunena kanthu mwamuna kungoti tondovi (chete), oti akafuna kukalipa, ngati akukalipira mwana.

Tsono mukati kuzungulira mutumukutanthauzanj?

Ayi, simisala, koma kupenga ndi chikondi, kotero kuti amayiwala banja lake ndipo mtima wake kumangokhala pa mkazi watsopanoyo basi, ngakhale akucheza ndi anzake pagulu mwadzidzi mudzamuwona dzambatuko—ndikupita, osadziwa kuti mkazi uja wakoka uta womuyitana kuti azipita ku nyumba. Mwachitsanzo, munthu wotere mudzamuwona akangoweruka ku ntchito munthu woti m'mbuyomu ankacheza ndi anzake, azingothamangira ku nyumba.

Kodi munthu kusintha makhalidwe nchifukwa?

Ayi, pali ndi kusintha kwake.

Tafotokozani zambiri za kondaine.

Si kanyama, koma ndi mankhwala; ena amatenga mchira wa buluzi [khala pakhomo]. Chimene chimachitika nchoti mkazi uja akafuna kudyetsa mwamuma wake amapita kwa sing'anga, ndiye sing'anga uja amamufunsa akufuna kondaine wamtundu wanji..., ngati akufuna kuti mwamuna wake asamayendeyende zili kwa iye. Pali zambiri zimene zimachitika koma zina za uve. Taganizani, nthawi zina akazi ena amatenga kaphukusi ka mapira nkumangirira kumalo obisika ngati mthete, ncholinga choti akamakodza mkodzo uja uzimeretsa mapira aja kenako asanduke chimera. Akatero ndiye amaphika thobwa nkusakaniza ndi chimera chija kumpatsa mwamuna wake, uku akunenerera, ndiye pali kondaine wina amadyetsa kwakwananda. Kondaine ameneyu ndi wachabe, chifukwa munthu wake samakonda kucheza ndi anzake, pamafika pena pake anzake akamamusinjilira kuti sayenda amvekere; ndakula, osadziwa kuti wadya kondaine. Pali akazi ena amatenga mthete kuviyika, madzi akewo kutsira mundiwo kumpatsa mwamuna. Mwachidule; chikondi choyendera kondaine ndi chachabe, chifukwa choti ngakhale mkazi aziyenda zake..., zachiwerewere mwamuna samanena kanthu, osadziwa kuti akumutengera Edzi, kenako udzamva kuti uje ampeza ndi kachirombo koyambitsa Edzi ali mkazi wake wamutengera.

Kodi thobwalo amamwa yekha?

Anthu ena atha kumwa nawo, koma siziwakhudza chifukwa wanenerera mwamuna wake yekha, komanso ndi pamene pagona zizimbapo.

Kodi kudyetsa mwamuna kondaine nkulakwa?

Kwabasi! Kulakwa kwenikweni, chifukwa kumavutitsa anthu osalakwa. Taganizani; munthu akangodya kondaine amayiwaliratu banja kuphatikizapo ana ake ndi achibale onse. Mwamuna wodyetsedwa kondaine, zochita zake zimasiyana ndi mmene ankakhalira poyamba. Nchifukwa chake, ndati kondaine ndi wachabe kaamba koti mwamuna akangodya ngati adali ndi banja lake amayiwala kulisamala, komanso ngati akufuna kutumiza thandizo, kaya chakudya amachita mozembetsa kuti mkazi wakeyo asadziwe, kumene kuli kulakwa, zotsatira zake ana amalephera kuphunzira. Inunso mwamva pagulu paja ena akupereka chitsanzo za mmene zidamuchitikira mkulu wina, yemwe adali ndi banja langwilo komanso lotsirilika, koma atayamba kupeza bwino adachita chibwenzi ndi mkazi wina koma adali kale ndi ana awiri, pamene iyeyo adali ndi ana anayi, komanso amawatumiza m'sukulu zapamwamba koti aliyense kumatsilira, koma atapeza chibwenzi, amati tsiku lina kugona komweko, mkazi uja adaganiza zofuna kulanda kenako adapita kwa sing'anga kukatenga kondaine. Anthu adangowona mkulu uja wasinthiratu zochita zake kotero kuti adayiwaliratu kusamala banja lake, nchifukwa chake ndanena kuti kudyetsa mwamuna kondaine nkulakwa.

Kodi mwamunayo amadziwa kuti wadya kondaine?

Sangadziwe kwa iye amangoti ndi chikondi

Tsono ngati kuli kulakwa, kodi wodyetsa kondaine akapulumuka?

Popeza kuti sindine Mulungu, koma ngati pali Lamulo loti konda mnzako monga uzikonda iwe mwini, ndiye kuti sakapulumuka chifukwa akuvutitsa anthu osalakwa. Nanga munthu akayiwale ana ake chifukwa cha mankhwala..., kuli bwino chikondi chizikhala chenicheni chofumira mumtima osati cha masalamusi, chifukwa chikondi cha mankhwala chili ngati cha ziwanda.

 

Advertise with us

Advertising that works wonders

Call +2651871181/070/563
or email: advertising@bnltimes.com