• Home
    • Advertisement
      Times Courier
  • Daily Times








    • dailytimesAdvertisement
  • Weekend Times
    • Advertisement
      sb
  • Malawi News
    • Advertisement
      qm
  • Sunday Times
    • Advertisement
      steers
  • E-Edition
  • Advertise
  • Contacts

Sat05182013

Last update01:14:09 PM

Back Malawi News Headlines Tikambe Boma liri ndi kampeni kumphasa—Mbowera

Boma liri ndi kampeni kumphasa—Mbowera

Patricia_Kaliati

Katswiri pa nkhani za ndale ku sukulu ya ukachenjede ya Mzuzu University a Noel Mbowela wati boma lili ndi zolinga polimbikira kuti makina omwe akutchedwa aukazitape (spy machine) ayambe kugwira ntchito.

Iwo adalankhula izi pamene Tikambe idafuna kudziwa maganizo awo pa za mmene makinawa atakhudzire moyo wa Amalawi.

"Chodabwitsa ndi chakuti m'dziko muno muli zinthu zambiri zomwe Amalawi akupanikizika nazo, mwachitsanzo; anthu amadandaula kuti akuberedwa pa mabilu a magetsi koma boma silidaganizepo zopeza njira yothetsera mchitidweu.

"Chifukwa chiyani boma langoganiza lero kuti likuyenera kuthandiza anthu kuti asamaberedwe ndi anthu opereka ntchito za lanya, mmalo moti boma liyambire pa nkhani za magetsi ndi madzi zomwe anthu akhala akuberedwa kwa nthawi yaitali.

"Chomwe ife tikudziwa ndi chakuti boma liri ndi zolinga zolakwikwa polimbikira kuti makinawa adzayambebe kugwira ntchito.

"Izi zikachitika ndiye kuti ufulu wa anthu wokhala ndi chinsinsi ukhala ukuphwanyidwa popeza pa ulamulo wa demokalase munthu akuyenera kukhala ndi ufulu wolankhula.

"Izi zithandizira kuti anthu andale agwiritse ntchito makinawa popeza zomwe anthu otsutsana nawo akulankhula ndikuwapezera mlandu polingalilanso kuti a polisi adawapatsa mphamvu yakupanga chipikisheni popanda kukhala ndi chilolezo zikungonjezera nkhawa pa mmene makinawa angamadzagwirire ntchito.

"Zomwe zingapereke chiopsezo kuufulu wa anthu , koma pali chiyembekezo chakuti anthu ena akufuna kukatenga chiletso ku bwalo la malamulo ndipo khothi ndi limene lingamasule za mmene makina amenewa angamadzagwirire ntchito,"a Mbowera adatero.

Nawonso a Dr Mustafa Hussein katswiri pa ndale ku sukulu ya ukachenjede ku Chancellor College wanena kuti makinawa antha kudzagwiritsidwa ntchito molakwika.

"Makina amenewa angathe kudzagwiritsidwa ntchito ndi anthu a ndale popezetsa adani awo mavuto chifukwa chomvera zina ndi zina zomwe anthuwo amakamba.

"Chomwe Amalawi tikuyenera kuchita ndi kugwirizana ndi kulipempha boma kuti makinawa lisawakhazikitse popeza angathe kudzetsa zovuta zochuluka kwa Amalawi ena popeza anthu a ndale atha kudzawagwiritsa ntchito pa zofuna zawo.

"M'dziko muno muli mavuto ochuluka omwe akufuna ndalama, mwachitsanzo vuto la kusowa kwa mafuta lomwe boma lingalichepetse pogwiritsa ntchito ndalama zomwe zikufuna kupita ku ntchito ya makinawo," a Hussein adatero.

Koma nduna yofalitsa nkhani za boma a Patricia Kaliati adati anthu omwe amapereka ntchito za lamya akupereka uthenga wolakwika kwa Amalawi pa nkhani ya makina omwe boma likufuna likhazikitse.

Izi zadza pambuyo pa uthenga omwe makampani a zalamya a MTL, TNM ndi ACL kutulutsa chikalata chomwe chikufotokoza kuti ngati makinawa angadzayambe kugwira ntchito ndiye kuti udindo wawo woonetsetsa kuti ufulu wa makasitomala awo wokhala ndi zinsinsi usazatheke.

A Kaliati adadzudzula makampaniwa kuti akungofuana kudyera masuku pamutu pa a A malawi pamene akulephera kupereka ntchito zapamwamba kwa makasitomala.

"Makampaniwa akugopereka magawo 25 pa magawo 100 pa ntchito zomwe adayenera kumapererka kwa Amalawi, ife tikufuna kuti iwo adzipereka magawo 100 onse omwe akuyenerera

"Makampaniwa ngati sangakwanitse kupereka ntchito zokwanira angosiya ndipo anzawo ena apezeka akuti angathe kukwanitsa

"Ife sitingonjera pa zofuna za makampaniwa, '' a Kaliati adatero.

Nalonso bungwe la Malawi Communications Regulatory Authority (MACRA) likuyesetsa kupereka mauthenga pa wailesi pofuna kudziwitsa komanso kuzindikiritsa Amalawi pa za mmene makinawa adzidzagwirira ntchito.

Mantha a anthu ochuluka ndi akuti makinawa angathe kudzachotsa ufulu wa anthu wokhala ndi chinsinsi pa zomwe akukamba pa lamya komanso ngakhale pa makina a intaneti.

 

Advertise with us

Advertising that works wonders

Call +2651871181/070/563
or email: advertising@bnltimes.com