• Home
    • Advertisement
      Times Courier
  • Daily Times








    • dailytimesAdvertisement
  • Weekend Times
    • Advertisement
      sb
  • Malawi News
    • Advertisement
      qm
  • Sunday Times
    • Advertisement
      steers
  • E-Edition
  • Advertise
  • Contacts

Thu05232013

Last update04:32:58 PM

Back Malawi News Headlines Tikambe Ndirande Hill ayibatiza

Ndirande Hill ayibatiza

Ndirande_Hill

Timu ya Ndirande CDSS idaphunzitsa a chiyamba kumene m'masewero a mpira wa miyendo wa amayi a Ndirande Hill Secondary School powabatiza ndi zigoli zitatu kwa ndanda m'chikho cha Matindi Womens' Football pa bwalo la Ndirande Hill la Mulungu Sabata latha.

Masewero omwe ankakomera mbali imodzi adayamba mochedwerapo popeza a Ndirande Hill ankafuna kulowetsa wosewera yemwe anzawo ankati sadali wophunzira wa pa sukuluyo.

Ndirande CDSS idayamba ndi mphamvu mwakuti zinkaoneka ngati mvula ya zigoli igwa patsikuli, koma sizidali chomwecho popeza atsikana a Ndirande Hill adayesetsa kutseka.

Zigoli ziwiri zidagoletsedwa m'chigawo choyamba pomwe chimodzi chidalowa mchigawo chomaliza.

Goli wa Ndirande Hill yemwe adaonetsa kuti kadali koyamba kuponya masewero a mpira wa miyendo wa amayi adali kulakwitsa zinthu zambiri koma mwayi udali wakuti otchinga awo adali kuyesetsa.

A Wilson Nyirenda omwe ndi mphunzitsi wa pa Ndirande Hill adanena kuti timu yawo sidachite bwino kaamba kakuti idalowetsa atsikana ena omwe adasewera koyamba.

"Tangonja kaamba kakuti tidalowetsa atsikana omwe kadali koyamba kusewera komanso omwe samabwera ku zokonzekera pa masewero.

"China ndi chakuti timu yathu sidagwirane popeza tangoyamba kumene kusewera masewerawa, koma ndili ndi chikhulupiliro kuti masewero omwe akubwerawo tidzachita bwino popeza taona zofooka zathu, " a Nyirenda adatero.

M'masewero ena omwe adachitika Sabata latha, Karibu Acadamy idachinya Saint Andrews 3 kwa 1, Matindi Private Secondary School idagonjetsa Ndirande Istitute Private Secondary School ndi zigoli 5 kwa 0, ndipo Poly Girls Idachinya Nyambadwe CDSS ndi zigoli 5 kwa 0.

 

Advertise with us

Advertising that works wonders

Call +2651871181/070/563
or email: advertising@bnltimes.com