• Home
    • Advertisement
      Times Courier
  • Daily Times








    • dailytimesAdvertisement
  • Weekend Times
    • Advertisement
      sb
  • Malawi News
    • Advertisement
      qm
  • Sunday Times
    • Advertisement
      steers
  • E-Edition
  • Advertise
  • Contacts

Sat05182013

Last update01:14:09 PM

Back Malawi News Headlines Tikambe Kinnah alowa tchire kusaka luso

Kinnah alowa tchire kusaka luso

Kinnah_Phiri_2

Kuyambira lolemba likubwerayi, phunzitsi wa timu ya mpira wa dziko lino Kinnah Phiri ayamba kupita ku m'madera a kumidzi kusakasaka anyamata osewera mpira wa miyendo kuti akayese nawo mwayi wosewera nawo mu mtima ya mpira ya dziko lino.

Kinnah adati wakhazikitsa ndondomekoyo atakhumudwa ndi momwe achinyamata omwe ali nawo mu mtimuyo adasewelera makamaka timuyo italephera kufika mu ndime yotsiliza ya chikho cha matimu a mu Africa pamene timuyo idali ndi mwayi wonse.

"Nthawi zambiri ndi madalira anyamata omwe amasewera matimu a supa ligi muno mu tawuni ndi ena omwe amasewera mmayiko a kunja zomwe sizidayende konse chaka chino. Pachifukwa chimenechi ndaganiza zoyang'ana ndekha luso m'madera akumidzi.

"M'madera aku midzi kuli luso lambiri koma limavuta kulipeza chifukwa achinyamatawa amanewa amakhala madera akutali ndi tawuni komanso sangakhale ndi mwayi wobwera kuno ku tawuni kudzasewera mpira chifukwa cha zovuta zosiyanasiyana. Ndichifukwa chake, ndaganiza zongowayendera ndekha basi," iwo adatero.

Kinnah adati iye ali ndi chikhulupiliro kuti ndondomekoyo iyenda bwino makamaka pa nthawi ino pamene masewero a mpira apita patsogolo kwambiri m'madera a kumidzi chifukwa cha kukhazikitsidwa kwa zikho zosiyanasiyana.

"Ndikupempha Amalawi nonse kuti mundithandize pamene ndikugwira ntchito imeneyi. Ntchito imeneyi siyanga ndekha ayi, koma ya tonse ife Amalawi. Ngati mukudziwa kuti wina wake ali ndi luso pena pake, ndiwuzeni kuti ndimupatse mpata wozayesa mwayi wake mu timuyi," iwo adatero.

 

Advertise with us

Advertising that works wonders

Call +2651871181/070/563
or email: advertising@bnltimes.com