Kwa anthu omwe akhala akugwira ntchito mumzinda wa Blantyre kwa zaka zochuluka kuona nkulu wina yemwe amayenda pa njinga yakapalasa pa ntchito yake ya umesinjala sichinthu chachilendo. Koma ambiri chomwe sakudziwa ndi chakuti kodi chinsinsi cha mkuluyi kuti adzikwanitsabe kupalasa njinga ngakhale zaka zake zili zochuluka chili pati? Mkulu yemwe tikumunenayi ndi a Frezer Ndau a zaka 71 zakubadwa ndipo kwao ndi ku Dedza kwa T/A Kachindamoto; iwowa amagwira ntchito ya umesinjala ndipo amapalasa njinga ngati simunthu wachikulire ngakhale ali ndi zaka zochulukirapo. Tikambe idachita chidwi ndi nkuluyi ndipo idamufunsa ndi mafunso kufuna kudziwa za chinsinsi chake.
Kodi ntchito ya umesinjala mudayamba liti?
Ine ntchito imeneyi ndidayamba 1966 ku Nzeru Radio ndipo njinga yoyamba ndidapatsidwa mu June. Ndipo ndidagwira ntchito ndi Nzeru Radio kufikira chaka cha 1984, pa 2 Febuluwale m'chaka cha 1984 ndidayamba kugwira ntchito ku Malawi Iron Steel Corperation Limited komwe ndidakagwira mpakana pano. Ine sukulu sindidachite kwambri ndidalekeza sitandade 3 m'chaka cha 1956, koma ndakhala ndikukondedwa ndi mabwana kaamba kokhulupilika pa ntchito.
Nanga akukumana ndi mavuto anji?
Ine pantchito yanga ya umesinjala ndakhala ndikukumana ndi mavuto ambiri, maka ndikamayenda pa nseu, ndingoyamika Mulungu kuti wakhala akunditeteza popeza sindidayambe ndachitako ngozi ya pa nseu muzaka zonse ndakhala ndikukwera njinga. Pali madilaivala ena omwe akaona wa njinga ya kapalasa samamuwerenga ngati ndi munthunso yemwe akuyenera kugwiritsa ntchito nseu kotero samapereka sizindikiro zakuti akukhota, enanso samamupatsa mpata wokwanira kotero mwina amangomuomba. Izi zimachititsa kuti ife okwera njinga za kapalasa tidzikhala pachiopsezo chogundidwa
Chinsinsi chawo chilipati?
Ine pa zaka zochuluka zomwe ndakhala pa ntchito ya umesinjala ndaphunzira kuti kukhulupirika pa ntchito ndi chinthu chamtengo wapatali. Ngakhale ndidali mesinjala koma mabwana anga akhala akundidalira kumakasiya ndalama kubanki. Ndipo zonse ndakhala ndikulongosola popanda kusokoneza kena kalikonse. Chinthu china ndi chakuti kuyendetsa njinga tsiku ndi tsiku zathandiza moyo wanga kukhala wa thanzi. Mabwana anga akhala akundinena kuti ndine chitsulo popeza sindidwaladwala. Zaka zonse ndakhala ndikugwira ntchito sindidagonekedweko m'chipatala. Chinsinsi china ndi chakuti ndakhala munthu odziletsa pa nkhani za azimayi. Ena amanena kuti mwamuna sayenera kumangodya nyemba zokhazokha koma amayenera kumasintha, kutathauza kuti osangodalira mkazi wa panyumba koma kumaona tina moyenda. Ine koma ndakhala ndikungodalira nyembazo kotero ndi chifukwa chake ndili wamphamvu komanso wa thanzi mpakana pano.
Malangizo
Ine ndikufuna kulangiza achinyamata amakono kuti akuyenera kukhala okhulupirika pa ntchito komanso kukhala ndi moyo wodzisunga popeza khwangwala wa mantha adafa ndi ukalamba. Langizo lina kwa achinyamata ndi lakuti akuyenera kupewa moyo wotolatola pa ntchito pofuna kuti alemere mwansanga, adziwe kuti magwiragwira amapha manja komanso ichi chakoma icho chakoma pusi adagwa chagada. Komanso langizo kwa oyendetsa galimoto pa nseu ndi lakuti adzitiganizira ife anthu oyenda pa kapalasa popeza ndifenso oyenera kugwiritsa ntchito nseu.

Advertisement







