• Home
    • Advertisement
      Times Courier
  • Daily Times








    • dailytimesAdvertisement
  • Weekend Times
    • Advertisement
      sb
  • Malawi News
    • Advertisement
      qm
  • Sunday Times
    • Advertisement
      steers
  • E-Edition
  • Advertise
  • Contacts

Tue05212013

Last update02:53:42 PM

Back Malawi News Headlines Tikambe Uzimba wa mbalame umafunika khama

Uzimba wa mbalame umafunika khama

Mlendo atatsikira pa siteji ya Lirangwe m'boma la Blantyre, angadabwe kuwona mavenda atanyamula malichero odzaza ndi mbalame zophikaphika, munthuyo nkumaganiza kuti mwina zikuphedwa ku Lirangwe komweko. Koma katswiri wodziwa uzimba wa mbalame Enock Benard wa m'mudzi mwa Masanjala, m'dera la Mfumu Lundu, m'boma la Blantyre akuti mbalame sizichokera kumeneko.

Ngati mukuti mbalame sizichokera kuno, nchifukwa chiyani ziri mpweche?

Zitha kukhala mpweche chomwechi kaamba koti akatswiri odziwa kupha mbalamezo ali kuno [Lirangwe], ndiponso ambiri amachokera mudzi uno wa Masanjala ndi wa Tepeka. Mwachidule; mmene mukucheza nanenu mudziwe kuti mukucheza ndi namandwa popha mbalame.

Kodi mudayamba liti uzimbawu?

Tidayamba m'chaka cha 1994, poyamba timagwilira konkuno m'madimba muli tsekera lambiri kenako zidayamba kutha, choncho tidayamba kupita madera ena, monga ku Chikhwawa, Nsanje, Balaka, Mwanza, Salima, Ntcheu ndi ku Neno, kumeneko kuli amnzathu amene amatipezera madimba mmene muli mbalame, tsono akapeza amatiyimbira foni kutidziwitsa, ndiye timapita. Choncho tikapha mbalame zambiri timabwera nazo kudzagulitsa, nchifukwa chake mavenda ambiri amakamba zoti mbalame zimachokera ku Lirangwe, osadziwa kuti zikuchokera kutali, kwa iwo kuti afunse kumene zikuchokera alibe nazo kanthu bola azipeza.

Kodi mumakonzekera bwanji popita ku uzimba?

Timatenga bigiri, mbale imodzi, mpoto wophikira nsima (popeza ndiwo zake kawirikawiri zimakhala utaka kapena kanyenya), kapu ndi mchere komanso maukonde awiri. Tikafika m'mudzi muja timapita kwa nyakwawa kukayidziwitsa kuti talowa m'mudzi mwake kudzapha mbalame, timachita izi kuti chitavuta china chake tiwone kopita. Ndiye akatilola timayenda m'mphepete mwamtsinje kuti tiwone malo amene akugona mbalame, tikawapeza basi timamanga kansakasa, kuphika chakudya chathu kudya, tikatha kudya timagawana ntchito, anyamata anayi amakhala kutsogolo, awiri amanyamula ukonde kumayang'anizana, m'mbali mwa ukonde timayikamo ndodo kuti mbalame zikalowamo tizizikulungiza.

Tafotokozani mumazigwira bwanji?

Anthu anayi amalowa pa tchirepo, ena awiri amakhala kutsogolo ndiye ama amayimba likhwelu kuwawuza anzawo aja kuti ayambe kusaka mbalame zija pokuwa, mmenemo titatambasula ukonde uja, poti zithawe zimalowa mu ukonde muja, kenako timakulungiza ukondewo kuti zisatuluke. Timatenga thumba, nkuloza kukamwa kwa ukonde uja, kuti tikamapha zizigwera m'thumbamo, kenako timatambasula ukonde uja nkulizanso likhwelu kuti ayambe kusaka, chokhachokhacho mpaka mbanda kucha. Nthawi zina zikayenda bwino timapha mbalame zokwanira 2,000 kapena 3,000 malinga ndi tchire lake. Tsono mmawa timanyamula kubwera nazo kudzagulitsa.

Mbalame mwabwera nazo kuno, nanga amasosola ndani?

Mavenda pamodzi ndi amayi akangomva kuti tabwera amakhala chire kuyembekezera, mavenda akagula mbalame zija amawapatsa amayi kuti azisosole ndikudula mitu popeza malipiro ake ndi mitu yomwe amapanga ndiwo, koma ngati atatopa ndi kudya mitu nawonso amangogulitsa. Ndikhulupilira mmene mumabwera kuno mwawona nthenga za mbalame m'mindamu.

Poti njoka zina zimakonda kukhala pamene pali mbalame, tsono mumadziwa bwanji kuti pa tchirepo pali njoka?

Patchire pamene pali njoka sipangagone mbalame, chifukwa zimachita mantha; mnzawo akangogwidwa basi zonse zimathawa. Inunso mukudziwa pamene pali njoka, aliyense asanadziwe mbalame ndi zimene zimadziwa msanga, ndipo mudzamvera kulira; si, si, chiki, chiki, cheke, cheke, ndiye mumadziwa kuti apa pali njoka kapena chirombo.

Koma nzowonadi mbalame zimene anthu akudyazi sizikuchokera ku kuno--Lirangwe?

Zowona wina asakunamizeni, kuno madimba adatha kalekale, ndipo ndikunena kaamba koti ndi geni yathu. Taganizani; kuchokera 1994...? Mwachitsanzo; sabata ya mawa tipita ku Mwanza ndi ku Neno chifukwa tatumiza kale mauthenga kumeneko.

Popeza pa chikuda pathu ena amadalira zizimba, inu mumatani?

Palibe zizimba zirizonse, timangopemphera kuti Ambuye atitsogolere ukhale ulendo wopambana wopanda 'minyama' matsoka basi.

 

Advertise with us

Advertising that works wonders

Call +2651871181/070/563
or email: advertising@bnltimes.com