Kafukufuku yemwe Tikambe yapanga wasonyeza kuti sikatundu yense yemwe wakwera mtengo kuchokera nthawi imene boma lidalengeza kuti mphamvu ya ndalama ya kwacha yagwa masabata awiri apitawo.
Tikambe
‘Sikatundu yense yemwe wakwera mtengo’
- 19 May 2012
- Justice Mponda
Kusiyana kwa kukhwima ndi kukhwimira
- 19 May 2012
- Stevie Bombeya
Chipatso kapena mbewu iliyonse makamaka chimanga chikafika podyeka amati chakhwima, koma mawu omwewo kumunena wina kuti "wokhwima iwe" amadana nazo kaamba koti amawona ngati wamuyalutsa, ndiye pali ena amakhwimira katundu, nanga zikusiyana pati? Nyakwawa Nzeru ya m'boma la Blantyre ikufotokoza kusiyana kwake motere:
Gogo akusalidwa kaamba ka ukalamba
- 19 May 2012
- Wyson Chiputa Gondwe
Kwa anthu ena ukalamba ndi nthawi yosangalala pozungulidwa ndi zidzukulu komanso kusangalala ndi mathandizo ochoka kwa ana omwe anabeleka. Koma kwa Gogo Esther NyamuNyirenda ukalamba ndi malodza popeza alibe zidzukulu komanso akusowa thandizo la tsiku ndi tsiku komanso anthu ena akuwasala.
Mawira: Dziwe la madzi otentha
- 14 April 2012
- Stevie Bombeya
M'boma la Nkhotakota m'mudzi mwa Tambala m'dera la Mfumu Malengachanzi muli malo ena amene amatulutsa madzi otentha ndipo anthu adawatcha malowa kuti Mawira (kutanthawuza madzi otentha). Anthu ena makamaka amayi mmalo mophitsa madzi oti amuna awo asambe amangopita kukatunga nkuyika ku bafa, kodi nanga chiyambi chake nchotani. Mfumu Malengachanzi ikufotokoza za chiyambi cha mawira motere:
Sindisunga mangawa—Pulezidenti Banda
- 13 April 2012
- Howard Mlozi
Pulezidenti Joyce Banda wati sasunga mangawa aliwonse kuchokera kwa munthu wina aliyense zomwe akhala akumunena, koma maso akhale kutsogolo kukonza dziko lino. Iye adalankhula izi Loweruka lapitali pomwe amamulumbiritsa ku Nyumba ya Malamulo ku Lilongwe.
Mabungwe awawuza apeze njira zambiri zopezera chithandizo
- 13 April 2012
- Howard Mlozi
Mabungwe omwe siaboma m'dziko akhoza kukhala pachiopso chachikulu cholephera kupitiliza ntchito zachitukuko ngati adalira njira imodzi yopezera thandizo monga ndalama zochokera kwa anthu akufuna kwabwino kapena mabungwe akumaiko akuja.
Nanazi zikusintha miyoyo ku Mulanje
- 13 April 2012
- Foster Benjamin
M'phephete mwa phiri la Mulanje kungoyenda pang'ono kuchokera mu nkhalango ya tiyi ya Minimini kuli mudzi waukulu wa Nande. Mudziwu, womwe wapangidwa ndi midzi ina yaing'onoing'ono monga Kholowa, Munyaka, Gawanya ndi ina, umabiriwira nthawi zonse ndi mbewu zosiyanasiyana zomwe anthu a mderali amalima.
Mabungwe, matimu amasewero alira Bingu
- 13 April 2012
- Howard Mlozi
Mabungwe kuphatikizapo matimu amasewero osiyana siyana m'dziko muno ati ndi okhudzidwa kwambiri ndi imfa ya mtsogoleli wakale wa dziko lino a Bingu Wa Mutharika omwe adamwalira mwadzidzi sabata latha.
Batile lisowa pa siteji ya Kawale
- 13 April 2012
- Auspicious Ndamuwa
Zinthu zina zikamachitika zimangokhala ngati nkhamba kamwa chabe. Pajatu sabata latha mkuluyu adakumana ndi mbwadza pomwe atsinzinantole ena adamubera chigubu cha mafuta pa siteji ya pa Mchesi pa ulendo wa usiku olowera ku Area 23. Itanyamuka pa Mchesi, minibasiyo idaimanso pa siteji ya pa Kawale 1. Shasha ndi dalaivala wakeyo adali kulirabe chifukwa chobetsa mafuta.
Amalawi ali ndi nkhawa—Cama
- 18 March 2012
- Justice Mponda
Bungwe lowona ufulu wa anthu ogula m'dziko muno la Consumers Association of Malawi (Cama) lati kuchedwa kwa boma kulengeza za kachulukidwe ka zokolora chaka chino kukubweretsa nkhawa pakati pa a Malawi.
‘Alimbikitsa ulimi wa nthilira’
- 18 March 2012
- Karen Msiska
Alimi a m'boma la Rumphi awalimbikitsa kuti ayambe ulimi wothilira pamalo amene akhoza kuchita ulimiwu.
Ndalama ya chikho cha Matindi ikwera
- 18 March 2012
- Steve Gulumba
Omwe akupereka ndalama yoyendetsera chikho cha Matindi Academy alonjeza kuti chaka chino chikhocho ndalama yake ikwera kuchoka pa K1.5 miliyoni kufika pa K3 miliyoni.
MSB ikhala yachitatu mu Countrywide
- 18 March 2012
- Mphatso Malidadi
Timu ya mpira wa miyendo ya MSB Socials yati yalimbikitsidwa pokhala yachitatu mu mpikisano wa Countrywide tournament womwe watha Sabata latha.
Girls Network: Kupereka chiyembekezo kwa atsikana
- 18 March 2012
- Howard Mlozi
Achinyamata amatengedwa kuti ndi atsogoleli amawa, koma kaamba kazovuta zomwe amakuna nazo pa moyo wawo watsiku ndi tsiku iwo amalephera kukwaniritsa masomphenya awo m'moyo. Mwachitsanzo, malingaliro awo odzakhala nzika zodalilika za dziko lino mtsogolo muno monga anamwino, atolankhani, asungi chuma komaso oweluza nkhani kumabwalo a milandu amamathera m'mlengalenga kaamba kazovuta zomwe amakumana nazo.
Shasha: 'Wantchito ayenera malipiro'
- 18 March 2012
- Auspicious Ndamuwa
"Adona, simungandipatse buluku limeneli ngati malipiro anga chikhalirecho tidagwirizana kuti mudzindipatsa makobiri... chimenechi nchibwana chamchombo lende!" Shasha adakalipa akumuyang'anitsitsa Khuruku ngati kadali koyamba kuti amuthire diso.
Kondaine: Mankhwala odyetsa amuna
- 18 March 2012
- Steve Bombeya
Masiku apitawa ndidakhala nawo pa zokambirana zokhudza matenda a Edzi m'boma la Neno, padali magulu angapo kotero kuti gulu lirilonse linkakambirana zokhudzana ndi kufala kwa Edzi, ena adati Edzi ikufala kaamba koti amuna kapena akazi ena amasiya maanja awo nkumachita zachisembwere. Pamene gulu lina lidati pali akazi ena amakonda kudyetsa amuna a eni kondaine. Choncho ndidafunsa Gogo Elina Kankhuni omwe adali m'gulu lokambirana za kondaine. Iwowa amachokera a m'mudzi mwa Donda II m'dera la Mfumu Chekucheku.
Boma liri ndi kampeni kumphasa—Mbowera
- 05 November 2011
- Steve Gulumba
Katswiri pa nkhani za ndale ku sukulu ya ukachenjede ya Mzuzu University a Noel Mbowela wati boma lili ndi zolinga polimbikira kuti makina omwe akutchedwa aukazitape (spy machine) ayambe kugwira ntchito.
Ndirande Hill ayibatiza
- 05 November 2011
- Steve Gulumba
Timu ya Ndirande CDSS idaphunzitsa a chiyamba kumene m'masewero a mpira wa miyendo wa amayi a Ndirande Hill Secondary School powabatiza ndi zigoli zitatu kwa ndanda m'chikho cha Matindi Womens' Football pa bwalo la Ndirande Hill la Mulungu Sabata latha.
Kinnah alowa tchire kusaka luso
- 05 November 2011
- Justice Mponda
Kuyambira lolemba likubwerayi, phunzitsi wa timu ya mpira wa dziko lino Kinnah Phiri ayamba kupita ku m'madera a kumidzi kusakasaka anyamata osewera mpira wa miyendo kuti akayese nawo mwayi wosewera nawo mu mtima ya mpira ya dziko lino.
Zaka 45 akukwera njinga
- 05 November 2011
- Steve Gulumba
Kwa anthu omwe akhala akugwira ntchito mumzinda wa Blantyre kwa zaka zochuluka kuona nkulu wina yemwe amayenda pa njinga yakapalasa pa ntchito yake ya umesinjala sichinthu chachilendo. Koma ambiri chomwe sakudziwa ndi chakuti kodi chinsinsi cha mkuluyi kuti adzikwanitsabe kupalasa njinga ngakhale zaka zake zili zochuluka chili pati? Mkulu yemwe tikumunenayi ndi a Frezer Ndau a zaka 71 zakubadwa ndipo kwao ndi ku Dedza kwa T/A Kachindamoto; iwowa amagwira ntchito ya umesinjala ndipo amapalasa njinga ngati simunthu wachikulire ngakhale ali ndi zaka zochulukirapo. Tikambe idachita chidwi ndi nkuluyi ndipo idamufunsa ndi mafunso kufuna kudziwa za chinsinsi chake.
Uzimba wa mbalame umafunika khama
- 05 November 2011
- Steve Bombeya
Mlendo atatsikira pa siteji ya Lirangwe m'boma la Blantyre, angadabwe kuwona mavenda atanyamula malichero odzaza ndi mbalame zophikaphika, munthuyo nkumaganiza kuti mwina zikuphedwa ku Lirangwe komweko. Koma katswiri wodziwa uzimba wa mbalame Enock Benard wa m'mudzi mwa Masanjala, m'dera la Mfumu Lundu, m'boma la Blantyre akuti mbalame sizichokera kumeneko.

Advertisement







